Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb17 tsamba 6-10
  • Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yosamutsa Likulu la Mboni za Yehova Komanso Ofesi ya Nthambi
  • Kodi Ntchito Yomanga Ikuyenda Bwanji ku Warwick?
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Gulu la Yehova Likupita Patsogolo
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Zinthu Zikuyenda ku Warwick
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku New York
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
yb17 tsamba 6-10
Pamalo olandirira alendo kulikulu la Mboni za Yehova ku Warwick, NY

Warwick, NY: Likulu la Mboni za Yehova Lapadziko Lonse

Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi

NGAKHALE kuti zinthu m’dziko la Satanali zikuipiraipira, atumiki a Yehova ali ndi ‘zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Malipoti otsatirawa akusonyeza zimene a Mboni za Yehova akhala akuchita posonyeza kuti ‘amakhulupirira Yehova, amachita zabwino komanso amayesetsa kukhala okhulupirika m’zochita zawo zonse.’​—Sal. 37:3.

Ntchito Yosamutsa Likulu la Mboni za Yehova Komanso Ofesi ya Nthambi

Ntchito yomanga maofesi atsopano mumzinda wa Wallkill ku New York inatha pa 1 February, 2016. Choncho Komiti ya Nthambi ya ku United States, Dipatimenti ya Utumiki komanso madipatimenti ena anasamukira kumalowa. Ntchito yomanga likulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse inatha ku Warwick moti anthu a m’banja la Beteli ya ku Brooklyn ayamba kusamukira kumalo atsopanowa.

Mapu a Beteli ya ku United States; maofesi a ku Wallkill; nsanja yaitali yomwe ili pamalowa komanso maofesi amangidwa ku Warwick

Kuyambira Lolemba pa 3 April, 2017, anthu azidzatha kupita kukaona malo atsopanowa. Poona mbali zitatu, anthu azidzayenda okha, koma poona mbali ina ya 4, azidzayenda ndi munthu wowasonyeza malo.

  1. Mbali ya “Dzina la Mulungu M’Baibulo” ili ndi Mabaibulo akale kwambiri omwe sapezeka masiku ano. Mbaliyi ilinso ndi umboni wosonyeza kuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo.

  2. Mbali ya “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova” ili ndi zithunzi zosonyeza mbiri ya Mboni za Yehova. Mbaliyi ikusonyezanso kuti Yehova wakhala akutsogolera, kuphunzitsa komanso kuthandiza anthu ake kuti azichita chifuniro chake mwadongosolo.

  3. Mbali ya “Likulu Lapadziko Lonse​—Anasonyeza Chikhulupiriro” ili ndi mavidiyo osonyeza mmene makomiti a Bungwe Lolamulira amathandizira kuti atumiki a Yehova azisonkhana, azilalikira, aziphunzira Mawu a Mulungu komanso azikondana.

Mbali zimenezi zizidzakhala zotsegula kuchokera Lolemba mpaka Lachisanu, kuyambira 8:00 koloko m’mawa mpaka 4:00 koloko madzulo. Mbali yomwe anthu azidzayenda ndi munthu wowasonyeza malo ija, izidzakhala ya maminitsi 20. Anthu azidzaona maofesi komanso panja pa Beteli. Azidzaona malo amenewa kuchokera Lolemba mpaka Lachisanu, kuyambira 8:00 koloko m’mawa mpaka 11:00 koloko komanso 1:00 koloko masana mpaka 4:00 koloko madzulo.

Musanapite kukaona malo, pitani pa jw.org. Onani pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAOFESI NDI KUONA MALO > United States.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena