Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 172
  • Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Mariya Mmagadala anali hule?
  • Kodi Mariya Mmagadala anali “mtumwi wa atumwi”?
  • Kodi Mariya Mmagadala anali mkazi wa Yesu Khristu?
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Ndinetu Kapolo wa Yehova!”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Sanafooke Chifukwa cha Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 172
Mariya Magadala ali patsogolo pa manda opanda kanthu ndipo wakumana ndi Yesu yemwe waukitsidwa.

Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?

Yankho la m’Baibulo

Mariya Mmagadala anali wotsatira wokhulupirika wa Yesu Khristu. Dzina lake lakuti Mmagadala liyenera kuti linachokera ku dzina la mzinda wotchedwa Magadala (kapena mwina lakuti Magadani). Mzindawu unali pafupi ndi nyanja ya Galileya. N’kutheka kuti pa nthawi inayake, Mariya ankakhala mumzindawu.

Mariya Mmagadala limodzi ndi azimayi ena angapo ankayenda ndi Yesu ndi ophunzira ake n’kumawathandiza kupeza zofunika pa moyo. (Luka 8:1-3) Iye anaona Yesu akuphedwa komanso anali pa gulu la anthu oyamba kumuona atangoukitsidwa.—Maliko 15:40; Yohane 20:11-18.

  • Kodi Mariya Mmagadala anali hule?

  • Kodi Mariya Mmagadala anali “mtumwi wa atumwi”?

  • Kodi Mariya Mmagadala anali mkazi wa Yesu Khristu?

  • Kodi Baibulo Limatchula anthu angati amene anali ndi dzina lakuti Mariya?

Kodi Mariya Mmagadala anali hule?

Baibulo silinena kuti Mariya Mmagadala anali hule. Zimene limanena zokhudza Mariya asanayambe kutsatira Yesu n’zakuti Yesuyo anamutulutsa ziwanda 7.—Luka 8:2.

N’chifukwa chiyani anthu ena amaganiza kuti iye anali hule? Zaka mahandiredi angapo Mariya atamwalira, anthu ena ananena kuti iye anali munthu (yemwe ayenera kuti anali hule) amene dzina lake silinatchulidwe koma anasambitsa mapazi a Yesu ndi misozi yake n’kuwapukuta ndi tsitsi lake. (Luka 7:36-38) Koma palibe umboni uliwonse m’Baibulo woti munthuyo anali Mariya.

Kodi Mariya Mmagadala anali “mtumwi wa atumwi”?

Ayi. Tchalitchi cha Katolika chimatchula Mariya kuti “Mariya Mmagadala Woyera” komanso “mtumwi wa atumwi” chifukwa choti anali woyamba kuuza atumwi kuti Yesu anaukitsidwa. (Yohane 20:18) Koma mfundo imeneyi siitanthauza kuti Mariya anali mtumwi ndipo Baibulo silinena paliponse kuti iye anali mtumwi.—Luka 6:12-16.

Baibulo linamaliza kulembedwa cha m’ma 98 C.E. Koma atsogoleri a matchalitchi sankamulemekeza kwambiri Mariya Mmagadala mpaka m’zaka za m’ma 500 C.E. Nkhani zina zimene zinalembedwa m’zaka za m’ma 100 ndi 200 C.E., zomwe sizinaphatikizidwe m’Baibulo, zimafotokoza kuti atumwi ena a Yesu ankachitira nsanje Mariya. Koma nkhani zimenezi ndi zabodza ndipo sizili m’Malemba.

Kodi Mariya Mmagadala anali mkazi wa Yesu Khristu?

Ayi. Baibulo limasonyeza kuti Yesu sanakwatire.a

a Onani nkhani yakuti “Kodi Yesu Anakwatira? Kodi Anali ndi Abale Ake?”

Kodi Baibulo Limatchula anthu angati amene anali ndi dzina lakuti Mariya?

Baibulo limatchula akazi 6 amene anali ndi dzina lakuti Mariya.b

  1. 1. Mayi ake a Yesu.—Mateyu 1:18.

  2. 2. Mchemwali wa Marita ndi Lazaro.—Yohane 11:1, 2.

  3. 3. Mariya Mmagadala.—Luka 8:2.

  4. 4. Mayi ake a Yakobo ndi Yose.—Mateyu 27:56.

  5. 5. Mayi ake a Yohane Maliko.—Machitidwe 12:12.

  6. 6. Mkhristu wa ku Roma amene anachitira zinthu zabwino zambiri mpingo wa kumeneko.—Aroma 16:6.

b Dzina lakuti Mariya ndi dzina la Chigiriki la dzina la Chiheberi lakuti Miriamu, lomwe linali dzina la mchemwali wa Mose.—1 Mbiri 6:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena