Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwhf nkhani 30
  • Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu
  • Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene muyenera kudziwa
  • Zimene mungachite
  • Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amaonera Zolaula
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Ndingapewe Bwanji Kuona Zithunzi Zolaula?
    Galamukani!—2007
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuonerera Zolaula?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Zithunzi Zolaula N’zowononga
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Mfundo Zothandiza Mabanja
ijwhf nkhani 30
Mwamuna yemwe akuoneka wokhumudwa wakhumata pamene mkazi wake wayang’ana kumbali mokhumudwa.

MFUNDO ZOTHANDIZA BANJA | OKWATIRANA

Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu

Mkazi wake anatulukira zimene mwamuna wake ankachita mobisa. Ndipo anapepesa kwambiri ndi kulonjeza kuti sadzachitanso. Ndipo anasiyadi kwa nthawi ndithu, koma kenako anayambiranso, ndiye chinangokhala chizolowezi chake choti akamupeza basi amangopepesa.

Kodi ndi nanunso mukukumana ndi zimenezi? Ngati ndi choncho, dziwani mmene chizolowezi choonera zolaula chingakhudzire mkazi wanu komanso zimene mungachite kuti musiyiretu chizolowezi chimenechi.a

Nkhaniyi ikufotokoza:

  • Zimene muyenera kudziwa

  • Zimene mungachite

  • Ngati mwamuna wanu amaonera zolaula

Zimene muyenera kudziwa

Kuonera zolaula kungasokoneze banja lanu. Kungachititse munthu yemwe munakwatirana nayeyo kuti azikhumudwa ndipo angasiye kukukhulupirirani.b

Mkazi amene mwamuna wake amaonera zolaula angamavutike ndi maganizo awa:

  • Anapusitsidwa. Mkazi wina dzina lake Sarah anati, “Ndinkamva ngati kuti mwamuna wanga wakhala akuchita chigololo maulendo ambirimbiri.”

  • Kudzimva kuti ndi operewera. Mkazi wina ananena kuti chizolowezi cha mwamuna wake choonera zolaula chinamupangitsa kudziona kuti “ndine wosaoneka bwino komanso zimandichititsa manyazi.”

  • Kusakhulupirirana. “Ndimakayikira chilichonse chimene mwamuna wanga akuchita,” anatero mkazi wina dzina lake Helen.

  • Nkhawa. Mkazi wina dzina lake Catherine anati, “Nthawi zonse ndimangokhalira kudera nkhawa za khalidwe la mwamuna wanga.”

Zoti muganizire: Baibulo limauza mwamuna kuti azikonda mkazi wake. (Aefeso 5:25) Kodi zingakhale zomveka mwamuna atamanena kuti amakonda mkazi wake koma amachititsa mkazi wakeyo kukhumudwa chifukwa cha chizolowezi chake choonera zolaula?

Zimene mungachite

Munthu amene amakonda kuonera zolaula amavutika kusiya khalidwe limeneli. Mkazi wina dzina lake Stacey, anati: “Mwamuna wanga anasiya kusuta fodya, marijuana komanso kumwa mowa, koma zikumuvutabe kusiya kuonera zolaula.”

Ngati zimenezi zimakuchitikirani, malangizo otsatirawa angakuthandizeni kusiyiratu khalidwe limeneli.

  • Dziwani chifukwa chake kuonera zolaula ndi koipa. Kuonera zolaula kumapangitsa kuti munthu akhale ndi khalidwe lodzikonda n’kumaganiza kuti akhoza kumadzisangalatsa yekha pa nkhani yogonana. Koma zimenezi zimachititsa kuti asamasonyeze makhalidwe othandiza kuti banja likhale losangalala monga kukondana, kukhulupirirana komanso kudalirana. Kuchita zimenezi ndi kusalemekeza Yehova Mulungu amene Anayambitsa banja.

    Lemba lothandiza: “Ukwati ukhale wolemekezeka.”​—Aheberi 13:4.

  • Vomerezani kuti muli ndi vuto. Musamanene kuti, ‘Si bwenzi ndi kuonera zolaula zikanakhala kuti mkazi wanga amandikonda kwambiri.’ Si bwino kuimba mlandu mkazi wanu kuti ndi amene wachititsa kuti muonerenso zolaula, chifukwa chakuti anachita zinthu zimene zinakukhumudwitsani.

    Lemba lothandiza: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.”​—Yakobo 1:14.

  • Muzinena zoona kwa mkazi wanu. Mwamuna wina dzina lake Kevin anati: “Ndimalankhulana ndi mkazi wanga tsiku lililonse. Ndimamufotokozera ngati ndinayang’anitsitsa chithunzi chodzutsa chilakolako chogonana kapena ngati ndinapewa kuyang’anitsitsa. Kulankhulana naye zoona pa nkhani imeneyi kumapangitsa kuti asamaganize kuti ndimamubisira zinazake.”

    Lemba lothandiza: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

  • Muzikhala osamala. Mukhoza kupezeka kuti mwayambiranso kuonera zolaula ngakhale patapita zaka zambiri mutasiya khalidweli. Kevin, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ndinasiya kuonera zolaula kwa zaka 10 ndipo ndinkaganiza kuti ndinathana nalo vutoli. Koma chizolowezi chimenechi chinali chisanatheretu, ndipo chinali ngati chilombo chomwe chabisala kuti chindivulaze.”

    Lemba lothandiza: “Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.”​—1 Akorinto 10:12.

  • Mukamayesedwa, dekhani. Ngakhale kuti simungaletse kukhala ndi chilakolako chofuna kuonera zolaula, mukhoza kusankha kuchita mogwirizana ndi mmene mukumvera kapena ayi. Chilakolako chimatha kuchoka mwinanso mwamsanga ngati muyesetsa kuika maganizo anu pa zinthu zina.

    Lemba lothandiza: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake m’njira yoyera kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana.”​—1 Atesalonika 4:4, 5.

  • Muzipewa zinthu zimene zingakuchititseni kuti muyambirenso kuonera zolaula. Buku lina la mutu wakuti Willpower’s Not Enough, linati: “Ngati muli pamalo oipa, ndiye kuti muli ndi machesi. Mukungofunika mafuta basi . . . kuti muyatse moto.”

    Lemba lothandiza: “Musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.”​—Salimo 119:133.

  • Musataye mtima. Zingatenge nthawi yaitali ngakhale zaka kuti mkazi wanu ayambirenso kukukhulupirirani. Koma anthu ambiri akwanitsa kuchita zimenezi.

    Lemba lothandiza: “Chikondi n’choleza mtima.”​—1 Akorinto 13:4.

Mwamuna ndi mkazi wake akucheza atakhala pansi uku atagwirana manja.

a Ngakhale kuti nkhani ino ikukamba za amuna, mfundo zimene zafotokozedwazi zingathandizenso akazi amene amaonera zolaula.

b Anthu ena okwatirana amanena kuti akamaonera limodzi zolaula zimalimbitsa banja lawo. Komabe, khalidwe limeneli si logwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.​—Miyambo 5:15-20; 1 Akorinto 13:4, 5; Agalatiya 5:22, 23.

Ngati mwamuna wanu amaonera zolaula

Musadziimbe mlandu. Musaganize kuti ndiye kuti ndinu munthu wosafunika, wosaoneka bwino kapenanso woperewera. Palibe mkazi amene angakwanitse kukhutiritsa chilakolako cha kugonana chobwera chifukwa choonera zolaula. Ndipo nthawi zambiri chilakolako chimenechi chimakhala chowonjeza komanso chosemphana ndi zimene angachite mwachibadwa.

Kodi mungathandize mwamuna wanu kuti akhale munthu amene mungayambirenso kumukhulupirira? Zingatheke, makamaka ngati mwamunayo akuyesetsa kuti asiye kuonera zolaula. Mkazi wina dzina lake Felicia anathandiza mwamuna wake kudziwa zimene zimamuyambitsa kuonera zolaula komanso zimene akuyenera kuchita kuti apewe khalidweli. Iye anati: “Ndikudziwa kuti vutoli la mwamuna wanga, osati langa. Koma ndinamuthandiza kuti asiye khalidweli, ndipo zimenezi zinathandizanso banja lathu.”​—Mlaliki 4:9-12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena