Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 102
  • Kodi Ndisiye Sukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndisiye Sukulu?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa chake anthu ena amasiya sukulu
  • Ganizirani zotsatirapo zake
  • Zimene zingathandize
  • Kodi Ndisiye Sukulu?
    Galamukani!—2010
  • Bwanji Ndingosiya Sukulu?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Zimene Mungachite Ngati Simukusangalalanso ndi Sukulu
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuika Nzeru Kumaphunziro Pasukulu?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 102
Mnyamata wanyansidwa ndipo wakweza dzanja lake pochoka kusukulu komanso kwa ophunzira anzake.

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndisiye Sukulu?

“Ndimadana ndi sukulu.” Ngati mumamva chonchi, mwina mungafune kuisiya. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zimene zingakuthandizeni pa nkhaniyi.

  • Chifukwa chake anthu ena amasiya sukulu

  • Ganizirani zotsatirapo zake

  • Zimene zingathandize

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Chifukwa chake anthu ena amasiya sukulu

Zifukwa zimene aphunzitsi amapereka ndi izi:

  • Kusakhoza bwino. ‘Ndimangolephera kusukulu.’

  • Mphwayi. ‘Ndikuona kuti zimene ndikuphunzira n’zosathandiza.

  • Umphawi. Ndimafunika kugwira ntchito kuti ndizithandiza banja lathu.

Ganizirani zotsatirapo zake

Baibulo limati: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngati mukuganiza zosiya sukulu, muyenera kuganizira zotsatirapo zake.

Dzifunseni kuti:

  • ‘Ndikasiya sukulu, kodi ndidzatha kupeza ntchito mosavuta m’tsogolo?’

    “Uziganizira za kupeza ntchito komanso mwina kusamalira banja lako m’tsogolo. Kodi udzachita bwanji zimenezi ngati mabwana ambiri amafuna kulemba ntchito anthu amene amaliza sukulu?​—Julia.

  • ‘Ndikasiya sukulu, kodi ndidzatha kuthana ndi mavuto amene ndingadzakumane nawo m’tsogolo?’

    “Sukulu imathandiza munthu kukonzekera zimene angadzakumane nazo pa moyo. Zinthu zimene ungadzakumane nazo zidzakhala zofanana ndi zimene unakumana nazo kusukulu, kaya ndi anthu amene ungadzakumane nawo, mayesero kapena ntchito imene uzidzagwira.”​—Daniel.

  • ‘Ndikasiya sukulu, kodi ndidzakhala ndi maluso amene ndingadzafunike m’tsogolo?’

    “Panopa ungaganize kuti maphunziro akusukulu ndi osathandiza koma ukadzakhala ndi zaka 23 ndipo ukupanga bajeti, udzaganiza kuti, ‘Ndinkachita bwino kukonda masamu.’”​—Anna.

Zimene zingathandize

  • Pemphani ena akuthandizeni. Baibulo limati: “Pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.” (Miyambo 11:14) Ngati simukukhoza bwino kusukulu, mupemphe makolo, aphunzitsi, alangizi akusukulu kapena wachikulire wina wodalirika kuti azikuthandizani.

    “Uziuzako aphunzitsi ako ngati zikukuvuta. Nthawi zina, ungaganize kuti vuto ndi aphunzitsi, koma nthawi zambiri ukapempha kuti azikuthandiza umayamba kuchita bwino.”​—Edward.

  • Ganizirani phindu lake. Baibulo limati: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.” (Mlaliki 7:8) Mukamaliza sukulu, mudzakhala mutaphunzira zambiri monga makhalidwe abwino komanso maluso, osati maphunziro anu okha.

    “Mwina sudzafunika kulemba nkhani kapena kukonzekera mayeso ukadzakula. Koma mmene umachitira zinthu ukapanikizika kusukulu zimakuthandiza kukonzekera mavuto amene udzakumane nawo ukadzamaliza sukulu.”​—Vera.

    Mnyamata akutsika boti lisanafike padoko. Anzake komanso aphunzitsi ake akumuchenjeza kuti asachoke.

    Kusiya sukulu kuli ngati kutsika boti lisanafike padoko. Mukhoza kudandaula kuti mwatsika mofulumira.

  • Ganizirani zina zimene mungachite. Baibulo limati “Wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Musafulumire kuganiza kuti kusiya sukulu ndi chinthu chokhacho chimene mungachite. Mwina mungamalize sukulu kunyumba pogwiritsa ntchito intaneti kapena njira ina.

    “Kusukulu umaphunzira kugwira ntchito mwakhama, kuthetsa mavuto komanso kugwirizana ndi anthu ena. Zinthuzi zidzakuthandizani moyo wanu wonse. Ndi bwino kuyesetsa kumaliza sukulu.”​—Benjamin.

Mfundo yofunika kwambiri: Mukamaliza sukulu mudzakhala wokonzeka kusamalira maudindo amene munthu wamkulu amakhala nawo.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Annabelle.

“Ukafunsira ntchito, nthawi zambiri mabwana amaganiza zokulemba ntchito ngati wamaliza sukulu. Kumaliza sukulu kumasonyeza kuti umachita khama kumaliza zimene wayamba. Kusiya sukulu si nzeru.”​—Annabelle.

Cole.

“Nthawi zina, sukulu imavuta ndipo ungaone kuti ndi bwino kungoisiya. Koma moyo wako wonse uzidzakumana ndi zinthu zovuta ndipo ukufuna kukhala munthu amene angathane nazo. Sukulu imakukonzekeretsa kuti udzathe kuchita bwino monga munthu wamkulu.”​—Cole.

Brynn.

“Ukakula, mwina sudzafunika kupeza yankho la samu yovuta. Koma uzidzafunika kugawa bwino nthawi, kumaliza zinthu pa nthawi yake komanso mwina kudzuka mofulumira. Sukulu ingakuthandize kuphunzira kuchita zinthu zimenezi.”​—Brynn.

Mfundo zobwereza: Kodi Ndingachite Bwino Kusiya Sukulu?

  • Ganizirani zotsatirapo zake. Ganizirani zimene zingadzachitike m’tsogolo ngati mwasiya sukulu. Mwachitsanzo, kodi mudzatha kupeza ntchito mosavuta, kukhala ndi maluso ofunika kapena kupirira mavuto?

  • Pemphani ena akuthandizeni. Ngati simukukhoza bwino kusukulu, mupemphe makolo, aphunzitsi, alangizi akusukulu kapena wachikulire wina wodalirika kuti azikuthandizani.

  • Ganizirani phindu lake. Kusukulu mumaphunzira zinthu zambiri osati maphunziro anu okha. Imakuthandizani kudziwa kuphunzira, kumaliza zinthu pa nthawi yake komanso kusamalira maudindo.

  • Ganizirani zina zimene mungachite. Ngati pa zifukwa zina muyenera kusiya kupita kusukulu, ganizirani zinthu zina zimene mungachite monga kuphunzira sukulu pa intaneti kapena m’njira ina.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena