Pamwamba kumanzere: Marek M. Berezowski/Anadolu Agency via Getty Images; pansi kumanzere: Halfpoint Images/Moment via Getty Images; pakati: Zhai Yujia/China News Service/VCG via Getty Images; pamwamba kumanja: Ismail Sen/Anadolu Agency via Getty Images; pansi kumanja: E+/taseffski/via Getty Images
KHALANI MASO!
Chaka cha 2023 Chinali Chodetsa Nkhawa Kwambiri—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
M’chaka cha 2023, padzikoli panachitika zinthu zambiri zomwe zinali umboni wakuti tikukhala m’nthawi imene Baibulo limanena kuti ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Taonani mmene zinthu zomwe zikuchitika masiku ano zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo.
Zimene Baibulo limanena zokhudza zochitika zapadzikoli
“Nkhondo ndi malipoti a nkhondo.”—Mateyu 24:6.
“Zachiwawa zikuwonjezereka m’madera ambiri padziko lapansili.”a
Onani nkhani yakuti “Ndi Ndani Angateteze Anthu Wamba Pankhondo?” komanso “Ndalama Zankhaninkhani Zoposa $2 Trillion Zikugwiritsidwa Ntchito Pogulira Zida Zankhondo Padziko Lonse.”
“Zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana.”—Maliko 13:8.
“Kungoyambira kumayambiriro kwa chaka cha 2023, padzikoli pakhala pakuchitika zivomerezi zokwana 13 zoopsa kwambiri ndipo chiwerengerochi n’chapamwamba kwambiri pa zivomerezi zomwe zakhala zikuchitika pa chaka.”b
Onani nkhani yakuti “Ku Turkey ndi ku Syria Kwachitika Zivomerezi Zoopsa.”
“Kudzaoneka zinthu zoopsa.”—Luka 21:11.
Takhala tikunena kuti dziko likutentha; koma pano tayamba kunena kuti dziko likuwira.”—António Guterres, UN secretary-general.c
Onani nkhani yakuti “Nyengo Yotentha Modabwitsa M’chaka cha 2023—Kodi Baibulo Limanena Zotani?.”
“Kudzakhala njala.”—Mateyu 24:7.
“2023 ndi chaka chinanso chodetsa nkhawa kwambiri kwa anthu omwe amapeza movutikira kuti apezere mabanja awo chakudya.”d
Onani nkhani yakuti “Vuto la Kusowa kwa Chakudya Padziko Lonse Chifukwa cha Nkhondo ndi Kusintha kwa Nyengo.”
“Nthawi yapadera komanso yovuta.”—2 Timoteyo 3:1.
“Munthu mmodzi pa anthu 8 alionse padzikoli ali ndi vuto linalake lamaganizo.”e
Onani nkhani yakuti “Achinyamata Ambiri Akuvutika Ndi Matenda Amaganizo.”
Kodi tiyembekezere zotani mu chaka cha 2024?
Palibe amene anganeneretu kuti m’chaka cha 2024 mudzachitika zakutizakuti. Koma zomwe zikuchitika padzikoli zikusonyezeratu kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma lakumwamba lilowa m’malo maboma onse a anthu ndipo boma limeneli lidzathetsa mavuto ndi nkhawa zonse zimene anthu ali nazo.—Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:4.
Pamene tikuyembekezera kuti zimenezi zichitike, tizidalira Mulungu kuti azitithandiza. Baibulo limanena kuti:
“Ndikamachita mantha, ndimadalira inu.”—Salimo 56:3.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira Mulungu? Tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zimene Baibulo limalonjeza zokhudza tsogolo lopanda mavuto. Mungayesere kuphunzira Baibulo mokambirana kwaulere kuti muone mmene inuyo ndi banja lanu mungapindulire ndi zimene Baibulo limalonjeza.
a Foreign Affairs, “A World at War: What Is Behind the Global Explosion of Violent Conflict?” by Emma Beals and Peter Salisbury, October 30, 2023.
b Earthquake News, “Year 2023: Number of Major Earthquakes on Course for Record,” May, 2023.
c United Nations, “Secretary-General’s Opening Remarks at Press Conference on Climate,” July 27, 2023.
d World Food Programme, “A Global Food Crisis.”
e World Health Organization, “World Mental Health Day 2023,” October 10, 2023.