Anton Petrus/Moment via Getty Images
KHALANI MASO!
Kodi Nkhondo Yapadziko Lonse Ichitika Posachedwapa?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Pa zaka 30 zapitazi, anthu ambiri akhala akuona kuti mayiko ambiri tsopano ayamba kugwirizana ndipo zinthu zikuyendako bwino padziko lonse. Komabe, zimene zakhala zikuchitika posachedwapa zikusonyeza kuti zinthu zayamba kusinthanso.
“Anthu akuda nkhawa poganiza kuti nkhondo ya ku Gaza ikhoza kukhudza mayiko enanso chifukwa dziko la Israel ndi gulu la Hezbollah ayamba kumenyana kumalire a dziko la Lebanon.”—Reuters, January 6, 2024.
“Dziko la Iran likubweretsa chiopsezo m’mayiko a azungu ndipo panopa likugwirizana ndi dziko la Russia ndi China. Dziko la Iran layambiranso kupanga zida za nkhondo za nyukiliya.”—The New York Times, January 7, 2024.
“Dziko la Russia likupitirizabe kuphulitsa mabomba m’dziko la Ukraine.”—UN News, January 11, 2024.
“Dziko la China likutukuka pa nkhani za chuma ndiponso popanga zida za nkhondo, nalonso dziko la Taiwan layamba kutchuka. Komanso pali kusamvana pakati pa dziko la China ndi United States, zonsezi zikuchititsa kuti pakhale chiopsezo cha nkhondo.”—The Japan Times, January 9, 2024.
Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya kusamvana kumeneku? Kodi kungayambitse nkhondo yapadziko lonse?
Baibulo linalosera zochitika za masiku ano
Baibulo silinatchule mwachindunji za nkhondo iliyonse yomwe ikuchitika masiku ano. Komabe, linalosera za nkhondo zimene zikuchulukirachulukirabe masiku ano ndipo linaneneratu zokhudza “kuchotsa mtendere padziko lapansi.”—Chivumbulutso 6:4.
Buku la Danieli linalosera kuti “mu nthawi yamapeto,” mayiko amphamvu padziko lonse ‘adzakankhana’ kapena kulimbirana ulamuliro. Kulimbanaku kukuphatikizapo kugwiritsa ntchito mphamvu zazikulu pa nkhondo komanso kuwonongerapo “chuma” kapena ndalama zambirimbiri.—Danieli 11:40, 42, 43.
Kukubwera nkhondo
Baibulo limasonyeza kuti padziko lonse, zinthu zisanayambe kuyenda bwino, zidzayamba zaipa kwambiri. Yesu analosera kuti “kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko mpaka lero, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21) “Chisautso chachikulu” chimenechi chidzayambitsa nkhondo yotchedwa Aramagedo, yomwe imafotokozedwa kuti ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’—Chivumbulutso 16:14, 16.
Komabe, Aramagedo idzapulumutsa anthu a mitundu yosiyanasiyana, m’malo mowawononga. Mulungu adzagwiritsa ntchito nkhondo imeneyi pothetsa maulamuliro onse a anthu, omwe abweretsa nkhondo zoopsa padzikoli. Kuti mudziwe mmene Aramagedo idzabweretsere mtendere wosatha, werengani nkhani zotsatirazi: