KHALANI MASO
Kodi Kukhala Mkhristu Kumatanthauza Chiyani?—Zimene Baibulo Limanena
Masiku ano anthu ambiri padzikoli amadzitchula monyadira kuti ndi Akhristu, koma ngakhale zili choncho iwo amachita zinthu zopweteka anzawo. Anthu ena ndi adyera, osakhulupirika komanso osaganizira anzawo. Enanso amakhala osakhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wawo. Zochita zawozi zimachititsa kuti anthu ena azifunsa kuti: ‘Kodi kukhala Mkhristu kumatanthauza chiyani kwenikweni?’
Zimene kukhala Mkhristu kumatanthauza
N’zosavuta kuti munthu angonena kuti ndi Mkhristu. Koma zimenezi sizokwanira. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, Mkhristu ndi munthu amene ndi wophunzira wa Yesu Khristu. (Machitidwe 11:26) Yesu mwini wakeyo ananena kuti: “Mukapitiriza kusunga mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.” (Yohane 8:31) N’zoona kuti palibe amene angatsatire ndendende malangizo a Yesu osalakwitsa chilichonse. Komabe Mkhristu amayesetsa kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa ndipo amasonyeza zimenezi kudzera n’zimene amachita tsiku lililonse. Ganizirani zitsanzo zotsatirazi.
Akhristu amasonyeza ena chikondi chenicheni
Zimene Yesu ananena: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana choncho. Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.”—Yohane 13:34, 35.
Zimene Yesu anachita: Yesu anasonyeza chikondi chenicheni kwa anthu onse posatengera kuti ndi olemera kapena ayi, otchuka kapena ayi komanso kumene akuchokera. Iye anachiritsa odwala, anadyetsa anjala ndipo anafika ngakhale popereka moyo wake chifukwa cha anthu ena.—Mateyu 14:14-21; 20:28.
Zimene Akhristu amachita: Akhristu amasonyeza chikondi chenicheni mwa kukhala owolowa manja, opanda tsankho komanso amakhululukira ena. Iwo amathandiza anthu amene akufunika thandizo ndipo amalolera kusiya zinthu zimene n’zofunika kwa iwowo kuti athandize anthu ena.—1 Yohane 3:16.
Akhristu amakhala owona mtima
Zimene Yesu ananena: “Ine ndine . . . choonadi.”—Yohane 14:6.
Zimene Yesu anachita: Yesu anali woona mtima pa chilichonse chimene ankachita komanso kulankhula. Sanapusitsepo anthu kuti achite zofuna zake kapena kukhulupilira zinthu zabodza. Iye ankadziwika kuti ndi woona mtima, ngakhale pamene kuchita zimenezi kunkachititsa kuti azitsutsidwa.—Mateyu 22:16; 26:63-67.
Zimene Akhristu amachita: Akhristu sanama. Iwo amapereka misonkho, samaba komanso amagwira ntchito mwakhama kuti zigwirizane ndi malipiro amene amapatsidwa pa tsiku. (Aroma 13:5-7; Aefeso 4:28) Samabera ena mwachinyengo, saonera mayeso komanso kulemba zinthu zabodza pafomu yofunsira ntchito kapena zinthu zina.—Aheberi 13:18.
Akhristu amachita zinthu mokoma mtima
Zimene Yesu ananena: “Bwerani kwa ine inu nonse amene mukugwira ntchito yotopetsa ndi olemedwa ndipo ndidzakutsitsimulani. Senzani goli langa ndipo lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa ndipo mudzatsitsimulidwa. Chifukwa goli langa ndi losavuta kunyamula ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Zimene Yesu anachita: Yesu ankachita zinthu mokoma mtima ndipo ankachititsa kuti anthu azimufikira mosavuta. Ankalandira ana, ankalimbikitsa anthu omwe ali ndi nkhawa komanso ankalemekeza anthu ena.—Maliko 10:13-15; Luka 9:11.
Zimene Akhristu amachita: Akhristu amalankhula ndi ena mokoma mtima, iwo salankhula mwachipongwe kapena monyoza. (Aefeso 4:29, 31, 32) Iwo amaganizira anthu ena komanso amafufuza mipata yoti awathandizire.—Agalatiya 6:10.
Akhristu amakhala okhulupirika kwa mkazi kapena mwamuna wawo
Zimene Yesu ananena: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Maliko 10:9.
Zimene Yesu anachita: Ngakhale kuti Yesu sanakwatire, ankalimbikitsa anthu okwatirana kuti azikhala okhulupirika kwa wina ndi nzake. (Mateyu 19:9) Iye anachenjeza anthu kuti azipewa zinthu zimene zingasokoneze ukwati wawo.—Mateyu 5:28.
Zimene Akhristu amachita: Akhristu amapewa kuchita zinthu zimene zingachititse kuti ukwati ukhale wosalemekezeka. (Aheberi 13:4) Anthu okwatirana amakondana komanso kulemekezana.—Aefeso 5:28, 33.