Photo by Stringer/Getty Images
KHALANI MASO
Nkhondo Imene Ikuchitika ku Middle East—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Anthu padziko lonse ali ndi nkhawa ndi zomwe zingachitike chifukwa cha nkhondo imene ikuchitika pakati pa United States, Israel ndi Iran. Kodi nkhondo imeneyi ikula n’kukhudza mayiko ambiri? Kodi maboma angakwanitse kuthetsa nkhondo n’kukhazikitsa mtendere padzikoli?
Mwina anthu amene amadziwa ulosi wa m’Baibulo angamaganize kuti nkhondo imene ikuchitika ku Middle East ndi chiyambi cha nkhondo ya Aramagedo imene imatchulidwa m’buku la Chivumbulutso.
Kodi Baibulo limanena zotani?
Kodi maboma angathetse nkhondo imene ikuchitika ku Middle East?
Baibulo limanena kuti: “Musamakhulupirire anthu olemekezeka kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.”—Salimo 146:3.
Sitikudziwa ngati maboma angakwanitse kubweretsa mtendere m’mayiko amenewa. Komabe Baibulo limanena momveka bwino kuti palibe mtsogoleri wandale, boma kapena gulu la anthu limene lingakwanitse kuthetsa nkhondo n’kubweretsa mtendere padzikoli. Mulungu yekha ndi amene angakwanitse ‘kuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.
Kuti mumve zambiri, werengani Nsanja ya Olonda yakuti “Kodi Nkhondo Idzathetsedwa Bwanji?”
Kodi nkhondo ya ku Middle East ikukwaniritsa ulosi?
Baibulo limanena kuti: “Mudzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo. . . . Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.”—Mateyu 24:6, 7.
Nkhondo imene ikuchitika ku Middle East ndi chimodzi mwa zinthu zimene zikuyenera kuchitika “mapeto a nthawi ino” ndipo ndi umboni wosonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ (Mateyu 24:3; 2 Timoteyo 3:1) Nkhondo zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti posachedwapa Mulungu athetsa nkhondo ndi mavuto ena amene anthu akukumana nawo.
Kuti mumve zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha ‘Masiku Otsiriza’ Kapena Kuti Nthawi ‘ya Mapeto’ N’chiyani?”
Kodi nkhondo ya Aramagedo idzayambira ku Middle East?
Baibulo limanena kuti: “Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼChiheberi amatchulidwa kuti Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:16.
Nkhondo ya Aramagedo si nkhondo yapakati pa maboma a anthu imene idzayambikire ku Middle East. Koma ndi nkhondo yapadziko lonse imene idzachitike pakati pa maboma a anthu ndi Mulungu.
Kuti mumve zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?”
Kodi tingathane bwanji ndi nkhawa?
Baibulo limanena kuti: “Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse. Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu, muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza.”—Afilipi 4:6.
Yehovaa Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye. Chifukwa choti iye amatifunira zabwino, angamvetsere mapemphero athu n’kutithandiza kuti tithane ndi nkhawa zimene tili nazo. (1 Petulo 5:7) Njira imodzi imene amachitira zimenezi si kungotithandiza kumvetsa chifukwa chake padzikoli pamachitika nkhondo, koma amatithandizanso kudziwa mmene nkhondozi zidzathere komanso zimene adzachite kuti anthu asamavutikenso.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kuti mumve zambiri zokhudza mmene Mulungu amatithandizira, werengani nkhani yakuti “Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?”
a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18.