Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 19
  • N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi kudzivulaza kumene tikukambirana m’nkhaniyi n’kutani?
  • N’chifukwa chiyani anthu ena amachita zimenezi?
  • Ngati muli ndi vutoli, kodi mungatani kuti musiye?
  • N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?
    Galamukani!—2006
  • Ndinasiya Ntchito ya Ndalama Zambiri
    Galamukani!—2010
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kudzivulaza?
    Galamukani!—2006
  • Mmene Mungathandizire Mwana Wanu Amene Amadzivulaza Mwadala
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 19

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?

  • Kodi kudzivulaza kumene tikukambirana m’nkhaniyi n’kutani?

  • N’chifukwa chiyani anthu ena amachita zimenezi?

  • Ngati muli ndi vutoli, kodi mungatani kuti musiye?

  • Kufunsa mafunso

  • Mafunso ofunika kuwaganizira

  • Malemba oti ndiziwakumbukira

Kodi kudzivulaza kumene tikukambirana m’nkhaniyi n’kutani?

Kudzivulaza kumene tikukambirana m’nkhaniyi ndi khalidwe lokonda kudzicheka mwadala. Kuwonjezera pa kudzicheka, anthu ena amadziwotcha kapenanso kudzimenya. Ngakhale kuti nkhaniyi ikufotokoza kwambiri za kudzicheka, mfundo zake n’zothandizanso kwa anthu amene amakonda kudzivulaza mwadala m’njira zina.

Mukudziwa zotani pa nkhaniyi: Kodi mfundo zotsatirazi n’zoona kapena zonama?

  1. Atsikana okha ndi amene amadzivulaza.

  2. Khalidwe lodzicheka ndi lotsutsana ndi lamulo la m’Baibulo la pa Levitiko 19:28, limene limati: “Musamadzicheke.”

Mayankho olondola:

  1. Zonama. Ngakhale kuti zikuoneka kuti anthu ambiri amene ali ndi vutoli ndi atsikana, anyamata ena nawonso amadzicheka kapena kudzivulaza m’njira zina.

  2. Zonama. Lemba la Levitiko 19:28 likunena za zimene zinkachitika pa mwambo wakale wa anthu olambira milungu yonyenga, osati khalidwe lokonda kudzivulaza limene tikukambirana m’nkhaniyi. Komabe, n’zomveka kuganiza kuti Mlengi wathu safuna kuti tidzidzivulaza mwadala.—1 Akorinto 6:12; 2 Akorinto 7:1; 1 Yohane 4:8.

N’chifukwa chiyani anthu ena amachita zimenezi?

Mukudziwa zotani pa nkhaniyi: Kodi ndi mfundo iti imene mukuganiza kuti ndi yolondola kwambiri?

Anthu amadzicheka chifukwa . . .

  1. chovutika maganizo.

  2. amakhala akufuna kudzipha.

Yankho lolondola: A. Anthu ambiri amene amadzivulaza sikuti amafuna kudzipha. Iwo amangodzivulaza pofuna kuti amveko bwino chifukwa chovutika maganizo.

Taonani zimene achinyamata ena omwe ali ndi vuto lodzicheka ananena.

Celia: “Ndikadzicheka, ndimamvako bwino.”

Tamara: “Zimandithandiza ndithu. Ululu umene ndimamva ndikadzicheka ndi wabwino poyerekeza ndi umene ndimamva ndikamavutika maganizo.”

Carrie: “Nkhawa zimandisowetsa mtendere. Ululu umene ndimamva ndikadzicheka umandithandiza kuti ndiiwaleko mavuto.”

Jerrine: “Nthawi iliyonse ndikadzicheka, ndimamva bwino kwambiri chifukwa ndimaiwaliratu mavuto anga onse.”

Ngati muli ndi vutoli, kodi mungatani kuti musiye?

Kupemphera kwa Yehova Mulungu kungakuthandizeni kwambiri kuti muthane ndi vutoli. Baibulo limati: “[Mumutulire] nkhawa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.”—1 Petulo 5:7, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Yesani izi: Yambani ndi mapemphero afupiafupi. Mwina mungapemphere mwachidule kwa Yehova kuti, “Chonde, ndithandizeni.” M’kupita kwa nthawi, mudzayamba kulankhula zambiri m’pemphero lochokera pansi pa mtima lopita kwa “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

Koma pemphero sikuti langokhala chinthu chimene chingakuthandizeni kuti mumveko bwino kwa nthawi yochepa. Pemphero ndi njira yodalirika imene mungalankhulire ndi Atate wanu wakumwamba, yemwe akukulonjezani kuti: “Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”—Yesaya 41:10.

Anthu ambiri amene anali ndi vuto lodzicheka anathandizidwanso atalankhula ndi makolo awo kapena munthu wamkulu amene iwowo amamukhulupirira. Taonani zimene atsikana atatu ananena atadziwitsa vuto lawoli makolo awo kapena anthu ena achikulire.

Kufunsa Mafunso

  • Diana, wazaka 21

  • Kathy, wazaka 15

  • Lorena, wazaka 17

Kodi unayamba kudzicheka uli ndi zaka zingati?

Lorena: Ndinayamba ndili ndi zaka pafupifupi 14.

Diana: Ndinali ndi zaka 18 ndipo ndinkadzicheka pa nthawi yotalikirana mosiyanasiyana. Nthawi zina ndinkadzicheka tsiku lililonse, kapena mlungu uliwonse kapenanso pa milungu iwiri iliyonse ndipo nthawi zinanso ndinkatha mwezi wathunthu ndisanadzicheke.

Kathy: Ndinayamba khalidweli ndili ndi zaka 14. Mpaka pano, nthawi zina ndimadzichekabe mwa apo ndi apo.

N’chifukwa chiyani unkadzivulaza?

Kathy: Ndinkavutika kwambiri ndi maganizo odziona kuti ndine wachabechabe. Ndinkaona kuti palibe munthu amene angafune kuti ndikhale mnzake.

Diana: Nthawi zina ndinkakhala ndi nkhawa kwambiri mpaka kufika podziona kuti ndine wosafunika. Maganizo amenewa ankakula kwambiri mumtima mwanga. Zikatero ndinkalusa koopsa mumtima mwanga ndipo ndinkaona kuti chinthu chabwino chimene ndingachite kuti ukaliwo uchoke n’kudzicheka basi.

Lorena: Ndinkavutika kwambiri maganizo kapena kukwiya zedi ngakhalenso kukhumudwa kwambiri popanda chifukwa chilichonse. Zikafika pamenepa ndinkangodziona ngati ndine chinyalala chachabechabe ndipo ndinkafufuza njira yondithandiza kuti maganizo amenewa achoke. Ndikasowa mtengo wogwira, nthawi zina ndinkangoona kuti ndikufunika kudzivulaza basi.

Kodi kudzivulaza kunkakuthandizani?

Diana: Ee, kunkandithandiza kwambiri. Ndinkamvako bwino ndipo zinkakhala ngati ndatula katundu wolemera kwambiri amene ndinasenza.

Kathy: Kudzivulaza kuli ngati kulira. Ndinkamva bwino ndikadzicheka ngati mmene anthu ena amamvera bwino akalira kwambiri.

Lorena: Kudzicheka kunkandithandiza. Magazi akamatuluka zinkakhala ngati mkwiyo ndi nkhawa zimene zinadzadza mumtima wanga zikutuluka pang’onopang’ono.

Kodi munkaopa kuuza anthu ena zimene munkachitazo?

Lorena: Ee. Ndinkaopa kuti anthu ena azidabwa kuti ndine munthu wotani. Komanso sindinkafuna kuti anthu ena adziwe mavuto anga.

Diana: Nthawi zambiri anthu ankandiuza kuti ndine wolimba mtima, ndipo ndinkafuna kuti anthuwo asasiye kukhulupirira zimenezi. Ndinkaona kuti ndikauza ena kuti andithandize, ndioneka ngati wolemphera.

Kathy: Ndinkaopa kuti anthu angayambe kuganiza kuti mutu wanga sukuyenda bwino, ndipo zimenezi zikanangowonjezera vuto langalo. Komanso ndinkaona kuti ndine wosafunika kwenikweni moti ndinali woyenera kumavutika ndi ululu chifukwa chodzicheka.

N’chiyani chinakuthandizani kuti musinthe?

Lorena: Ndinauza mayi anga zimene ndinkachitazo. Ndinapitanso kwa dokotala amene anandithandiza kuti ndisamavutike maganizo kwambiri. Nditachita zimenezi, nthawi zina ndinkazivulazabe mwa apo ndi apo, koma kuphunzira Baibulo mwandondomeko komanso pafupipafupi kunandithandiza kwambiri. Ndinayambanso kulimbikira kwambiri pogwira ntchito yolalikira uthenga wa m’Baibulo. Mwa apo ndi apo, mwina ndipitirizabe kuvutika ndi maganizo odziona kuti ndine wosafunika. Koma maganizo amenewa akabwera m’mutu mwangamu, ndiziyesetsa kuwachotsa.

Kathy: Mlongo wina wachikhristu amene ndi wamkulu kuposa ine ndi zaka pafupifupi 10, anazindikira kuti chinachake chikundisowetsa mtendere ndipo atandifunsa, ndinamuuza. Ndinadabwa kwambiri atandiuza kuti m’mbuyomo nayenso anali ndi vuto ngati langalo. Apa tsopano ndinamasuka n’kumuuza zonse chifukwa nayenso poyamba anali ndi vutoli. Komanso dokotala anathandiza kwambiri. Anathandizanso makolo anga kuti azimvetsa vuto limene linkandisowetsa mtendereli.

Diana: Tsiku lina ndikucheza kunyumba kwa banja lina limene ndinkagwirizana nalo kwambiri, bambo wa panyumbapo anazindikira kuti chinachake sichili bwino. Mwachifundo, anandifunsa kuti ndinene chimene chinkandisowetsa mtendere. Mkazi wake anandigwira mwachikondi n’kunditsamiritsa pachifuwa chake kenako anandikumbatira ngati mmene mayi anga ankandichitira ndili mwana. Ndinayamba kulira, ndipo nayenso mayiyu anayamba kulira. Zinali zovuta kwambiri kuti ndiwauze zoti ndakhala ndikudzivulaza kwa nthawi yaitali. Komabe, panopa ndikusangalala kuti ndinawauza ndipo ndinathandizidwa.

Nanga Baibulo linakuthandizani bwanji?

Diana: Baibulo landithandiza kuzindikira kuti sindingathane ndi vutoli pandekha. Ndinazindikira kuti ndikufunika thandizo la Yehova Mulungu.—Miyambo 3:5, 6.

Kathy: Ndimalimbikitsidwa komanso kutonthozedwa kwambiri ndikamawerenga Baibulo chifukwa ndimazindikira kuti uthenga wake ndi wochokera kwa Mulungu.—2 Timoteyo 3:16.

Lorena: Ndikapeza mavesi amene akundikhudza kwambiri, ndimawalemba m’buku langa n’cholinga choti ndiziwakumbukira mosavuta.—1 Timoteyo 4:15.

Kodi pali vesi linalake limene limakukhudzani kwambiri?

Diana: Ee. Lemba la Miyambo 18:1, lomwe limati: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” Nthawi zina ndimavutika kuti ndikhale ndi anthu ena, koma vesi limeneli limandithandiza kuzindikira kuti kudzipatula n’koopsa kwambiri.

Kathy: Mavesi awiri a m’Baibulo amene ndimawakonda kwambiri ndi Mateyu 10:29 ndi 31. Pamavesi amenewa Yesu ananena kuti Yehova Mulungu amadziwa ngakhale mpheta imodzi ikafa. Kenako Yesu anawonjezera kuti: “Musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.” Ngakhale masiku ano, ndikawerenga mavesi awiri amenewa ndimakumbukira kuti Yehova amaona kuti ndine wofunika kwambiri.

Lorena: Ndimakonda lemba la Yesaya 41:9, 10. Palembali, Yehova anauza anthu ake kuti: “Sindinakutaye. Usachite mantha, pakuti ndili nawe. . . . Ndikulimbitsa.” Mawu akuti “ndikulimbitsa” amandichititsa kuganizira za mpanda wolimba kwambiri womangidwa ndi miyala, womwe munthu sangathe kuuboola. Lembali limandikumbutsa kuti Yehova amandikonda kwambiri ndipo nthawi zonse adzapitiriza kundithandiza komanso kundipatsa mphamvu.

Mafunso ofunika kuwaganizira

  • Mukakhala wokonzeka kuuza ena za vuto lanu kuti akuthandizeni, kodi mungauze ndani?

  • Kodi mungamuuze zotani Yehova Mulungu pa vuto lanulo?

  • Kodi mungatchule zinthu ziwiri (kupatulapo kudzivulaza) zomwe mungachite kuti mumveko bwino mukakhala ndi nkhawa kapena mukamavutika maganizo kwambiri?

Malemba oti ndiziwakumbukira

Yesani izi: Mukamawerenga Baibulo kenako n’kupeza mavesi amene akukutsimikizirani zoti Yehova amakukondani kapena oti angakuthandizeni kuti muziona zolephera zanu kapena muzidziona nokha m’njira yoyenerera, alembeni. Mukhozanso kulemba mawu a mzera umodzi kapena ingapo osonyeza chifukwa chake mavesiwo angakuthandizeni. Pofuna kukuthandizani, taonani ena mwa mavesi amene anathandiza Diana, Kathy ndi Lorena.

  • Aroma 8:38, 39

    “Mavesi amenewa amandisonyeza kuti Yehova amandikonda, ngakhale zinthu zizioneka ngati sizikundiyendera bwino.”—Diana.

  • Salimo 73:23

    “Vesi limeneli komanso mavesi ena ofanana nalo amanditsimikizira kuti sindili ndekha. Zili ngati kuti Yehova ali pambali pangapa.”—Kathy.

  • 1 Petulo 5:10

    “Nthawi zina vutolo silingathe nthawi yomweyo. Tingafunikire kuvutika ‘kwa kanthawi.’ Komabe, Yehova angatithandize kuti tikhale olimba n’kupirira mayesero aliwonse.”—Lorena.

Malemba ena oti muwaganizire

  • Salimo 34:18

  • Salimo 54:4

  • Salimo 55:22

  • Yesaya 57:15

  • Mateyu 11:28, 29

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena