Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 93
  • Kodi Yesu Anaukitsidwa ndi Thupi Lotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Anaukitsidwa ndi Thupi Lotani?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kubweranso kwa Kristu—Kodi Kuwoneka Motani?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Chiukiriro
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Chiukiriro—Cha Yani, ndipo Kuti?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 93
Yesu akuonekera kwa Tomasi ndi ophunzira ena ali ndi mabala a misomali m’manja ake

Kodi Yesu Anaukitsidwa ndi Thupi Lotani?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limanena kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.”​—1 Petulo 3:18; Machitidwe 13:34; 1 Akorinto 15:45; 2 Akorinto 5:16.

Ngakhalenso Yesu anasonyeza kuti sadzaukitsidwa ndi thupi limene anali nalo. Ananena kuti: ‘Ndidzapereka mnofu wangawu kuti dzikoli lipeze moyo.’ (Yohane 6:51; Mateyu 20:28) Choncho ngati Yesu akanaukitsidwa ndi thupi lakelo, zikanakhala ngati sanapereke nsembe ya dipo. Koma izi si zimene zinachitika chifukwa Baibulo limanena kuti Yesu anapereka thupi ndiponso magazi ake nsembe “kamodzi kokha.”—Aheberi 9:11, 12.

Ngati Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu, ndiye zinatheka bwanji kuti ophunzira ake amuone?

  • Nthawi zina angelo amatha kudzichititsa kuti aoneke ngati anthu. Mwachitsanzo, kale angelo ena anaonekera kwa anthu ndipo anadya ndiponso kumwa limodzi ndi anthuwo. (Genesis 18:1-8; 19:1-3) Komabe anali adakali angelo moti kenako anasinthanso n’kupita kumwamba.​—Oweruza 13:15-21.

  • Nayenso Yesu ataukitsidwa anadzichititsa kuti aoneke ngati munthu kwa kanthawi. Koma popeza anali ndi thupi ngati la mngelo, Yesu ankatha kuonekera kwa anthu ndiponso kusowa mosadziwika bwino. (Luka 24:31; Yohane 20:19, 26) Ngakhale ndi choncho, sikuti nthawi iliyonse imene ankaonekera kwa anthu ankaoneka mofanana. N’chifukwa chake ophunzira ake ankamuzindikira chifukwa cha zimene ankanena kapena kuchita.​—Luka 24:30, 31, 35; Yohane 20:14-16; 21:6, 7.

  • Pa nthawi imene Yesu ankaonekera kwa mtumwi Tomasi, ankaoneka ngati munthu wokhala ndi mabala. Anachita zimenezi kuti athandize Tomasi chifukwa poyamba ankakayikira zoti Yesu waukitsidwadi.​—Yohane 20:24-29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena