Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 60
  • Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yomwa Mowa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yomwa Mowa?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ganizirani zimene zingachitike pambuyo pomwa mowa
  • Sankhani zochita
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhudza Mowa?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Mumayendera Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Mowa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Mungatani Kuti Musayambe Kumwa Mowa Mopitirira Malire?
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 60
Wachinyamata akupatsidwa mowa ndi anzake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yomwa Mowa?

Baibulo silimaletsa kumwa mowa pang’ono ngati malamulo akuvomereza kutero. Komabe limaletsa kuledzera.—Salimo 104:15; 1 Akorinto 6:10.

Kodi mungatani ngati mukukakamizidwa kuti mumwe pamene malamulo kapena makolo anu sakukulolani?

  • Ganizirani zimene zingachitike pambuyo pomwa mowa

  • Sankhani zochita

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Ganizirani zimene zingachitike pambuyo pomwa mowa

Anzanu ena angaganize kuti kumwa mowa n’kofunika kuti munthu asangalale. Koma kodi chingachitike n’chiyani pambuyo pomwa mowa?

  • Munthu ali m’ndende

    Kuphwanya malamulo. Potengera kumene mumakhala, ngati mutamwa mowa pamene malamulo sakukulolani kutero, mukhoza kulipira chindapusa, kuimbidwa mlandu, kulandidwa laisensi yoyendetsera galimoto, kupatsidwa chilango chogwira ntchito zosiyanasiyana m’dera lanu, kapena kutsekeredwa m’ndende kumene.—Aroma 13:3.

  • Foni

    Kuononga mbiri. Mowa umapangitsa munthu kuyamba kuchita zinthu mopanda manyazi. Chifukwa cha mowa, munthu akhoza kunena kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake akhoza kunong’oneza nazo bondo. (Miy. 23:31-33) Masiku ano zipangizo zamakono zachuluka kwambiri, choncho zomwe mungachite zingafalikire mosavuta ndipo zikhoza kukhudza mbiri yanu kwa nthawi yayitali.

  • Mkazi akuchitidwa zankhanza

    Kulephera kudziteteza. Kumwa mowa kungachititse kuti anthu ena akuchitireni nkhanza mosavuta komanso kukugwiririrani. Kungachititsenso kuti muzingoyendera maganizo a anzanu zimene zingakuikeni m’mavuto kapena kuchita zinthu zosemphana ndi malamulo.

  • Botolo la mowa lopanda kanthu

    Kukonda kwambiri mowa. Kafukufuku wina akusonyeza kuti munthu akayamba kumwa mowa ali wamng’ono kwambiri, n’zosavuta kuti azidalira kwambiri mowa akafuna kuchita zinthu. Kumwa mowa n’cholinga chofuna kuthana ndi kupanikizika maganizo, kusungulumwa kapena kuboweka ndi zinazake, kumayambitsa chizolowezi chimene kumakhala kovuta kwambiri kuchisiya.

  • Chigaza ndi mafupa

    Imfa. M’chaka china posachedwapa, munthu mmodzi ankafa pamaminitsi 52 aliwonse m’dziko la United States pangozi zochitika chifukwa choyendetsa galimoto munthu atamwa mowa. Nthawi inayake chaka chilichonse achinyamata oposa 1,500 osapitirira zaka 21 ankafa pangozi za galimoto chifukwa chomwa mowa. Izi zinachitika kwa zaka 5 zotsatizana. Ngakhale kuti inuyo simunamwe mowa, mukhoza kuika moyo wanu pangozi ngati mutakwera galimoto imene woyendetsa wake wamwa mowa.

Sankhani zochita

Mukhoza kupewa zinthu zoopsa zomwe zingachitike chifukwa chomwa mowa mosayenera ngati mutasankhiratu zimene mukufuna kuchita.

Mfundo ya M’Baibulo: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Ndi kupanda nzeru kumwa mowa kenako n’kumayendetsa galimoto kapena kuchita zina zake zimene zimafuna kuti munthu azichite akuganiza bwinobwino.

Chosankha: ‘Ndingamwe mowa pokhapokha ngati kuchita zimenezi sikukuphwanya malamulo komanso pamene zinthu zili bwino.’

Mfundo ya M’Baibulo: ‘Mumakhala akapolo a amene mumamumvera.’ (Aroma 6:16) Ngati mukumwa mowa chifukwa chakuti anzanu akumwa, ndiye kuti mukulola anzanuwo kuti azikusankhirani zochita. Ngati mukumwa mowa n’cholinga chofuna kuthana ndi kupanikizika kapena kuboweka, ndiye kuti simukudziphunzitsa luso lotha kulimbana ndi mavuto bwinobwino.

Chosankha: ‘Sindingalole kumwa mowa chifukwa choti anzanga akundikakamiza.’

Mfundo ya M’Baibulo: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” (Miyambo 23:20) Ngati anzanu ndi amakhalidwe oipa, sangamalemekeze zimene mwasankha. N’zosavuta kuyamba kumwa kwambiri mowa mukakhala ndi anzanu omwe ndi zidakwa.

Chosankha: ‘Anthu omwe amamwa mowa mwauchidakwa sangakhale anzanga apamtima.’

Zimene achinyamata anzanu amanena

Jordan

Jordan ananena kuti: “Pa nthawi imene ndinali kusukulu, anthu anayesetsa kundinyengerera kuti ndimwe mowa. Koma nthawi zonse ndinkadzikumbutsa zimene lemba la 1 Akorinto 15:33 limanena. Lembali limati: ‘Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.’”

Jenna

Jenna anati: “Ndimayesetsa kupewa anthu komanso zochitika zimene zingandipangitse kuti ndimwe mowa. N’zosangalatsa kuti ndili ndi anzanga amene amasankha bwino zinthu pa nkhani ya mowa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena