Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 92
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi zakudya zopatsa thanzi ndi zotani?
  • Ndingatani kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse?
  • Ndingatani Kuti Ndichepetse Thupi?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Ndingachepetse Motani Thupi?
    Galamukani!—1994
  • Kuthana ndi Vuto la Kunenepa Kwambiri
    Galamukani!—2012
  • Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 92
Mnyamata akusankha zakudya zoti adye mu firiji

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?

N’zosakayikitsa kuti mumadziwa zoti kusowa zakudya za magulu onse kukhoza kuwononga thanzi lanu. Ndipo munthu amene sadya zakudya zopatsa thanzi ali wamng’ono amachitanso zomwezo akadzakula. Choncho ndibwino kuti mukhale ndi chizolowezi chomadya zakudya zopatsa thanzi panopa.

  • Kodi zakudya zopatsa thanzi ndi zotani?

  • Ndingatani kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse?

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Kodi zakudya zopatsa thanzi ndi zotani?

Baibulo limatiuza kuti ‘tizichita zinthu mosapitirira malire,’ ndipo zimenezi zikuphatikizapo kudya. (1 Timoteyo 3:11) Choncho poganizira mfundoyi, ndibwino kudziwa kuti . . .

  • Tiyenera kudya zakudya za magulu onse. Pali magulu 5 a zakudya omwe ndi mkaka, mapuloteni, zipatso, masamba, ndi zakudya za m’gulu la chimanga ndi mpunga. Anthu ena amasiya kudya zakudya zina poopa kunenepa. Koma zimenezi zingachititse kuti thupi lanu lizisowekera zinthu zina zofunika.

    Tayesani izi: Fufuzani kapena funsani dokotala wanu kuti mudziwe ubwino wa zinthu zosiyanasiyana zomwe zimapezeka mu zakudya. Mwachitsanzo:

    Makabohaidireti angakupatseni mphamvu. Mapulotini amathandiza kuti thupi lanu lizilimbana ndi matenda komanso lizikula bwino. Zakudya zina za mafuta mukazigwiritsa ntchito moyenera, zingakuthandizeni kukhala amphamvu ndiponso kupewa matenda a mtima.

    “Ndimayesetsa kudya zakudya za magulu onse. Ndipotu sikulakwa kudyako switi imodzi kapena tizakudya tina tongosangalatsa m’kamwa. Koma sibwino kuti munthu azingokhalira kudya zinthu zimenezi. Umafunika kuti nthawi zonse uzidziikira malire n’cholinga choti uzidya za magulu onse.”—Brenda.

    Mnyamata akufuna kugwa pampando womwe uli ndi miyendo itatu

    Chakudya chimene chikusowekera zinthu zofunika m’thupi chili ngati mpando umene ukusowekera mwendo umodzi

  • Tizipewa kupitirira malire. Zimenezi zingaphatikizepo kusadya mokwanira, kudya kwambiri kapenanso kusiyiratu kudya zakudya zomwe munkazikonda.

    Tayesani izi: Onani mmene mwakhala mukudyera kwa mwezi umodzi. Ndiyeno dzifunseni kuti, ndi maulendo angati omwe munachita zinthu zomwe zatchulidwa pamwambazi? Nanga ndi zinthu ziti zimene mungasinthe n’cholinga choti muzidya moyenera?

    “M’mbuyomu, panali masiku ena omwe ndinkakonda kudya zakudya zopatsa mphamvu kwambiri pamene masiku ena ndinkayesetsa kuzipewa. Kenako ndinasiya kuganizira kwambiri kuchuluka kwa chakudya chopatsa mphamvu chimene ndikudya. Ndinkangoyesetsa kuti ndikangokhuta ndizisiya kudya. Zinanditengera nthawi ndithu koma panopa ndikuona kuti ndimadya moyenera.”—Hailey.

Ndingatani kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse?

  • Muzidziwiratu zakudya zomwe mukufuna kudya. Baibulo limanena kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” (Miyambo 21:5) Choncho kuti muzidya zakudya zopatsa thanzi muyenera kumadziwiratu zakudya zoyenera.

    “Kuti uzidya zakudya zabwino umafunika kukonzekera, ndipo nthawi zambiri zakudya zopatsa thanzi zimayenera kukonzedwa kunyumba. Ngakhale kuti zingaoneke zovuta, pamapeto pake zimathandiza ndipo zingachititse kuti musamawononge ndalama.”—Thomas.

  • Muzidya zakudya zopatsa thanzi m’malo mwa zosafunika. Baibulo limanena kuti: “Usunge nzeru zopindulitsa.” (Miyambo 3:21) Nzeru zopindulitsa zidzakuthandizani kupeza njira zopezera kapena kukonzera chakudya chabwino.

    “Tsiku lililonse ndinkasinthanitsa chakudya chimodzi chosafunika kwenikweni ndi chakudya chopatsa thanzi. Mwachitsanzo, m’malo modya switi ndinkadya apozi. Pasanapite nthawi, ndinayamba kudya zakudya zambiri zopatsa thanzi m’malo mwa zosafunika.”—Kia.

  • Musamayembekezere zimene simungakwanitse. Baibulo limanena kuti: “Ukadye chakudya chako mokondwera.” (Mlaliki 9:7) Kudya zakudya zopatsa thanzi sikukutanthauza kuti muzidya zakudya zosasangalatsa zokhazokha kapena kuti muziganizira kwambiri chakudya chilichonse chomwe mukudya. Ngakhale mutakhala kuti mukufuna kuchepetsa thupi, muzikumbukira kuti cholinga chanu n’kukhalabe wa thanzi. Choncho musamayembekezere zimene simungakwanitse.

    “Posachedwapa ndinachepetsa thupi langa ndi makilogalamu osachepera 14. Komabe pa nthawiyi sindinakhalepo osadya, ndinkadyabe zakudya zoyenera komanso sindinkadziimba mlandu ndikadya zakudya zina zotsekemera. Ndinazindikira kuti kuchepetsa thupi kumatenga nthawi ndipo ndinkangofunika kusintha zinthu pa moyo wanga.”—Melanie.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Delayna

“Njala ikandiwawa ndili koyenda, ndimapezeka kuti ndangogula zakudya zosayenera. Popewa zimenezi, ndimatengeratu chakudya changa chamasana kapena tizakudya tina kunyumba. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse.”—Delayna.

Andrew

“Mwina mukhoza kukhumudwa mukaona kuti anthu ena amangodya chakudya chilichonse popanda kukumana ndi vuto lililonse. Koma inuyo musamadziyerekezere ndi anthuwo. M’malomwake muzidziwa zakudya zomwe zingakuthandizeni inuyo n’kumayesetsa kudya zimenezo.”—Andrew.

Mfundo zobwereza: Kodi ndingatani kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi?

  • Muzidziwiratu zakudya zomwe mukufuna kudya. Muzikonzeratu chakudya chanu mukamapita koyenda m’malo mongogula chilichonse.

  • Muzidya zakudya zopatsa thanzi m’malo mwa zosafunika. Muzisunga tizakudya tina topatsa thanzi m’malo mosunga tchipisi ndi zakumwa zoziziritsa kukhosi.

  • Musamayembekezere zimene simungakwanitse. Musamadziyerekezere ndi anthu ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena