30 Yakobo ataona zimenezi anauza Simiyoni ndi Levi+ kuti: “Mwandiputira mavuto aakulu, ndipo mwandidanitsa ndi anthu amʼdziko lino, Akanani ndi Aperezi. Ine ndili ndi anthu ochepa. Iwowa ndithu asonkhana nʼkutiukira ndipo atitha tonse, ine ndi banja langa.”