18 Iye anati: “Ukufuna ndikupatse chikole chotani?” Mkaziyo anapitiriza kuti: “Mundipatse mphete ya udindo+ wanuyo ndi chingwe chake, ndiponso ndodo yanuyo.” Pamenepo iye anapereka zinthuzo kwa mkaziyo, nʼkugona naye ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera.