7 Yosefe ataona abale akewo, nthawi yomweyo anawazindikira, koma iye anayesetsa kuti asamuzindikire.+ Choncho analankhula nawo mwaukali nʼkuwafunsa kuti: “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera kudziko la Kanani, ndipo tabwera kudzagula chakudya.”+