21 Kenako iwo anayamba kukambirana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira mʼbale wathu uja.+ Pajatu tinaona mmene ankamvetsera chisoni pamene ankatichonderera kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamumvere. Nʼchifukwa chaketu takumana ndi tsoka limeneli.”