14 Koma Isiraeli anatambasula dzanja lake lamanja nʼkuliika pamutu pa Efuraimu, ngakhale kuti ndi amene anali wamngʼono. Anatambasulanso dzanja lake lamanzere nʼkuliika pamutu pa Manase. Anasemphanitsa dala manja ake chifukwa Manase ndi amene anali mwana woyamba.+