8 Patapita nthawi, anasamuka pamalopo nʼkupita kudera lamapiri, kumʼmawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga tenti yake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kumʼmawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe+ nʼkuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+