14 Choncho Abulamu anamva kuti mʼbale wake+ wagwidwa ndipo akupita naye kudziko lina. Atamva zimenezo iye anasonkhanitsa anyamata ake odziwa kumenya nkhondo. Anali atumiki ake okwanira 318, omwe anabadwira mʼnyumba yake. Iwo anatsatira adaniwo mpaka ku Dani.+