23 Choncho panopa lumbira pamaso pa Mulungu kuti udzakhala wokhulupirika kwa ine, kwa ana anga ndi kwa mbadwa zanga. Ndiponso kuti udzasonyeza chikondi chokhulupirika ngati chimene ine ndakusonyeza. Lumbira kuti udzasonyeza chikondi chimenechi kwa ineyo ndi anthu amʼdziko limene ukukhala.”+