36 Ndiyeno Esau anati: “Aka tsopano nʼkachiwiri akundichenjerera amene uja! Kodi si chifukwa chake dzina lake ndi Yakobo?+ Ukulu wanga anatenga kale,+ apa tsopano watenganso madalitso anga!”+ Iye ananenanso kuti: “Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?”