37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsa abale ake onse kuti akhale atumiki ake. Komanso ndamudalitsa kuti akhale ndi zokolola zambiri ndiponso vinyo watsopano wambiri.+ Nanga chatsalanso nʼchiyani choti ndikuchitire mwana wanga?”