18 Iwo adzamvera ndithu mawu ako+ ndipo iweyo ndi akulu a Isiraeli mudzapite kwa mfumu ya Iguputo nʼkukaiuza kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi+ walankhula nafe. Ndiye chonde mutilole kuti tiyende ulendo wamasiku atatu kupita mʼchipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’+