6 Choncho uwauze Aisiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndidzakupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani ndipo ndidzakulanditsani kuti musakhalenso akapolo awo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+