5 ndipo mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo adzafa.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa kapolo wamkazi amene akugwira ntchito pamphero ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+