39 Iwo anayamba kuphika mikate yozungulira yopanda zofufumitsa pogwiritsa ntchito ufa wokanda umene anachoka nawo ku Iguputo uja. Ufawo unalibe zofufumitsa chifukwa anawauza kuti achoke ku Iguputo mofulumira kwambiri moti sanathe kukonza chakudya chilichonse ponyamuka.+