24 Mundipangire guwa lansembe ladothi, ndipo muziperekapo nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zamgwirizano, nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu. Dziwani kuti mʼmalo onse amene ndachititsa dzina langa kukumbukiridwa,+ ndidzabwera kwa inu kumeneko ndipo ndidzakudalitsani.