41 Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira. Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa, nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.