27 Kenako iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Aliyense wa inu amange lupanga lake mʼchiuno. Ndiyeno mudutse mkati mwa msasa kuchoka pageti lina kufika pageti lina, ndipo aliyense wa inu aphe mʼbale wake, munthu wokhala naye pafupi ndi mnzake wapamtima.’”+