21 Kenako aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa,+ komanso aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa, anabwera ndipo anabweretsa zopereka kwa Yehova zoti zikagwire ntchito pachihema chokumanako ndi pa utumiki wonse wochitika pamenepo. Anabweretsanso zinthu zopangira zovala zopatulika.