22 Iwo anapitiriza kubwera, amuna pamodzi ndi akazi, aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa. Anabweretsa zokongoletsera zomanga pazovala, ndolo, mphete ndi zokongoletsera zina komanso zinthu zosiyanasiyana zagolide. Onse anapereka zopereka zawo zagolide kwa Yehova.+