-
Ekisodo 37:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse inali ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse inalinso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho anazipanga choncho.
-