17 Ndiyeno aziingʼamba pakati chamʼmapiko mwake, koma osailekanitsa. Kenako wansembe aziiwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nkhuni zimene zili pamoto kuti pakhale utsi. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa yoperekedwa kwa Yehova.’”