2 Akatero azibweretsa nsembe yakeyo kwa ana a Aroni, ansembe. Ndipo wansembe azitapa ufa wothira mafutawo pamodzi ndi lubani yense kudzaza dzanja limodzi, nʼkuuwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo.+ Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa yoperekedwa kwa Yehova.