31 Kenako azichotsa mafuta onse a mbuziyo,+ ngati mmene amachotsera mafuta a nsembe yamgwirizano.+ Akatero wansembe aziwotcha mafutawo paguwa lansembe kuti akhale kafungo kosangalatsa kwa Yehova. Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.