7 Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa, azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ kuti zikhale nsembe zakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+