15 “Munthu akachita mosakhulupirika pochimwira zinthu zopatulika kwa Yehova mosadziwa,+ azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake yakupalamula.+ Potchula mtengo wa nkhosayo azigwiritsa ntchito masekeli asiliva ofanana ndi sekeli lakumalo oyera.+