16 Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera, azilipira ndipo aziwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a malipirowo.+ Malipirowo aziwapereka kwa wansembe limodzi ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula, kenako wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo adzakhululukidwa.+