18 Azibweretsa kwa wansembe nkhosa yopanda chilema kuti ikhale nsembe yakupalamula.+ Mtengo wa nkhosayo uzikhala wofanana ndi mtengo wake woikidwiratu. Ndiyeno wansembe aziphimba machimo a munthuyo chifukwa cha cholakwa chimene anachita mosadziwa ndipo adzakhululukidwa.