15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi komanso azitengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, aziziwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo kuti zikhale kafungo kosangalatsa kwa Yehova.+