6 Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara kuti: “Musasiye tsitsi lanu osalisamala kapena kungʼamba zovala zanu+ kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire gulu lonseli. Abale anu omwe ndi nyumba yonse ya Isiraeli ndi amene alire anthu amene Yehova wawapha ndi moto.