13 Kenako azipha nkhosa yaingʼono yamphongoyo pamalo amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza,+ pamalo oyera. Azichita zimenezi chifukwa nsembe yakupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe yakupalamula ndi yopatulika koposa.+