-
Levitiko 14:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Koma ngati munthuyo ali wosauka ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi, azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi monga nsembe yakupalamula. Nsembeyo aziiyendetsa uku ndi uku kuti amuphimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake yambewu.
-