-
Levitiko 23:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Popereka nsembe imeneyi muziperekanso nsembe yambewu. Nsembeyo izikhala ufa wosalala wothira mafuta, muyezo wake magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.* Muziperekanso vinyo wa nsembe yachakumwa, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*
-