16 Ngati munthu wapereka mbali ina ya munda wake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, mtengo wa malowo uzikhala wogwirizana ndi mbewu zimene angadzalepo. Ngati angadzalepo balere wokwanira muyezo umodzi wa homeri, ndiye kuti mtengo wa malowo ndi masekeli asiliva 50.