20 Mbadwa za Rubeni, mwana woyamba wa Isiraeli,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo.