19 Wansembe azitenga mwendo wakutsogolo wa nkhosa yamphongo umene wawiritsidwa.+ Azitenganso mʼdengumo mkate woboola pakati wopanda zofufumitsa ndi kamkate kopyapyala kopanda zofufumitsa. Zinthuzi aziike mʼmanja mwa Mnaziriyo atameta chizindikiro cha unaziri wake.