25 Wansembe azikapereka nsembe yophimba machimo a gulu lonse la Aisiraeli. Akatero, anthuwo adzakhululukidwa+ chifukwa analakwitsa mosazindikira, komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova ndiponso apereka nsembe yamachimo kwa Yehova chifukwa cha zimene analakwitsazo.