18 Ndiyeno munthu amene si wodetsedwa+ azitenga kamtengo ka hisope+ nʼkukaviika mʼmadzimo kenako aziwaza tentiyo, ziwiya zonse ndi anthu onse amene anali mutentiyo. Komanso aziwaza munthu amene anakhudza fupa la munthu, munthu amene waphedwa, mtembo kapena manda.