5 Iye anatumiza anthu kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje wamʼdziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane kuti: “Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja afika kuno. Iwo adzaza dziko lonse lapansi+ kumene munthu angayangʼane, ndipo akukhala pafupi penipeni ndi dziko langa.